Ambiri tikondwera mwa Yesu,
Nanga inu, nanga inu?
Tapeza chipulumutso ndithu,
Nanga inu, nanga inu? ×2
(Chorus)
Masiku onse timakondwera,
Pakumva mawu ake a Yesu
Olalikira tidzamumvera
Nanga inu, nanga inu? ×2
(back to chorus)
Ife tiyembekezera Yesu,
Nanga inu, nanga inu?
Chimwemwecho chilli mumtimamu,
Nanga inu, nanga inu? ×2
(back to chorus)
Titasokera tinabwerera,
Nanga inu, nanga inu?
Tidziwa kuti ndiwo uchimo,
Nanga inu, nanga inu? ×2
(back to chorus)
Tinachoka munjira za imfa,
Nanga inu, nanga inu?
Takopeka ndi Mawu a Yesu,
Nanga inu, nanga inu? ×2
(Repeat chorus twice)