Kuli bwanji kwathu? Ndinafunsa, mlonda iye nati:
Usiku wapita ndithu, kwayandika kucha;
Usalire, yendabe ndi chiyembekezo chodala
Mpaka udzafika m’mwamba pa tsiku losatha.
2 Ndafunsa msrikali wa Khristu, iye nayimba nati:
Ndidzamenyanatu nkhondo patsala pang’ono.
Usalire, pirira kufikira nkhondo idzatha,
Pakuti olakika adzalandira mphotho.
3 Ndinafunsa dziko, nyanja ndi dzuwa izo zinati:
Nthawi ili kutha Yesu ali pafupitu,
Usalire, zizindikiro zili kuonekatu,
Chilengedwe chonse chilindira kudza kwake.