

Prompt / Lyrics
Odi Odi kuno, ife a Malawi Blood Transfusion Service, MBTS, abwezi anu pa nkhani ya kupereka magazi mwa ufulu wanu komaso mosakakamizodwa Tabweraso kukudziwitsani komaso kukumemani kuti abale athu muzipatalamu akulira usana ndi usiku kufunafuna thandizo la magzi tiyeni tichitepo kathu popereka magazi. Amayi oyembekezera , ana ang'ono ang'ono , anzathu amene anachita ngozi za pa mseu komaso abale athu amene akudwala matenda a cancer. Abale amenewa akusowerakera thandizo la magazi kuti akhaleso ndi moyo wina. Inu nonse amene zaka zanu zikuyambira 16 mpaka 65 zakubadwa ndipo mukulemera kuyambira 45 kgs mpaka mtsogolo tiyeni tipereke magazi kuti tipulumutse miyoyo ya abale athuwa. Tisazengereze koma tichitepo kanthu popereka magazi. Dziwani kuti dyereni ndi mwereni komaso ya transport, zilipo ndithu. Chonde chonde ngati timamwa mowa, tisamwe pobwera chifukwa timafuna mukhale ndi malingaliro komaso maganizo a mngwiro.
Tags
male, studio
1:41
No
4/7/2026