B.y.s.o.n(Byson)
Ena
Eya
Ena ena
Eya oo!
Mtima umawawa
Ngati waponda khala(lamoto)
Chiyembekezo chimathawa
Kuopa kulumidwa ndi chakuda
Nthanana zonse zimantha
Chimwemwe chija
Chasanduka misozi
Kuseka kuja
Kwasanduka kulira
Si sorry yense
Anasonyeza kugonja
Si misozi yonse
Imasonyeza kukhudzika
Ndimaonera pa social media
Anthu akukondana
Chondilimbitsa mtima
Sindikuchiona (ona)
Sindikuchiona (ona)
Pena ndimazimbitsa ( ine)
Kwinaku misozi ikutsika (ine)
Akalakwa iye
Amafuna ine ndimupepese
Pamau anga
Ma arguments mbwe!
Ngati sunakondepo munthu
Khala choncho
Kukonda munthu
Sichinthu chopweka
Ngati sunalimbe mtima
Ngati sunatsazike
Ngati sunakonzeke
Kukalowa mudziko lachikondi
Bwerera bwerera bwerera (bwerera)
Si sorry yense
Anasonyeza kugonja
Si misozi yonse
Imasonyeza kukhudzika
Ndimaonera pa social media
Anthu akukondana
Chondilimbitsa mtima
Sindikuchiona (ona)
Sindikuchiona (ona)
Chikondi chimafuna kufatsa
Kupupuluma, kukula mtima
Ndi Chikondi sizigwiriza
Pafupi pafupi kupepesana
Ngakhale sunalakwe (walakwa)
Mnzako mupepese
Chonsecho ndiwe mamuna
Anzako a akazi mbwe
Chonsecho ndi mkazi
Koma nzako a amuna mbwe
Ubwenzi sungasamale
Mulungu polenga Eva
Anamuuzitsa mamunako umumvere (obey)
Kwa mamunako udzipereke (submit)
Udzetse chimwemwe
Si sorry yense
Anasonyeza kugonja
Si misozi yonse
Imasonyeza kukhudzika
Ndimaonera pa social media
Anthu akukondana
Chondilimbitsa mtima
Sindikuchiona (ona)
Sindikuchiona (ona)
Amufe timakumana ndi zambiri
Physical struggle
Spiritual struggle
Mental struggle
Financial struggle
Kufika kunyumba
M'malo mopeza mtendere
Pomwe mavuto amachulukira
Ndiye n'kumati ulowera kuti?(ulowera kuti)
Ambiri asochela
Chifukwa chosaka Chikondi (chenicheni)
Ambiri alowa thengo
Chifukwa chosaka Chikondi (chenicheni)
Ambuye tithandizeni
M'masautso, muzowawa
Koma koma komaaaa
Si sorry yense
Anasonyeza kugonja
Si misozi yonse
Imasonyeza kukhudzika
Ndimaonera pa social media
Anthu akukondana
Chondilimbitsa mtima
Sindikuchiona (ona)
Sindikuchiona (ona)
Only you God knows
My everything is in your hands
Byson (b. Y. S. O . N)
Eya o ona
Eya uu ona
Eya ioa ona
Mtima limba
Tomorrow will be better than today