Ndimakukumbukirabe
(Chorus)
Papita nthawi koma ndimakukumbukirabe,
Mkazi wanga, moyo wanga,
Kusiyana kwathu, sikunali kwabwino inde ,koma
Ndikungopempha kuti tibwererane.
(Verse 1)
Ndikumakhala pano mosweka mtima Dearly,poti nthawi zonse ndimaganiza za iwe,
Nthawi yomwe tinakhala pamodzi m'chikondi ndi iwe,
Ndi kugwirizana, tikukondana,
Ngati ndikotheka udzakhaleso nane, course am ready now!.
(Chorus)
Papita nthawi koma ndimakukumbukirabe,
Mkazi wanga, moyo wanga,
Kusiyana kwathu, sikunali kwabwino inde,koma
Ndikungopempha kuti tibwererane.
(Verse 2)
Zinthu ndinaziipitsa, kusiyana chifukwa cha zazing’ono?
Kuwonenga kwanga, ndingathe kukonza am ready,
Chikondi chachikulu, chimayenda mu mtima,
Kupanda umodzi, si umoyo, koma chilango.
(Chorus)
Papita nthawi koma ndimakukumbukirabe,
Mkazi wanga, moyo wanga,
Kusiyana kwathu Dearly, sikunali kwabwino inde, koma
Ndikungopempha kuti tibwererane.
(Bridge)
Bwerabwera!!!, anthu atikumbukire,
Moyo wanga wakhala wopanda ntchito,
Nthawi zonse popanda iwe,
Tilimbikitse, chikhumbo cha mtima wanga.
(Chorus)
Papita nthawi koma ndimakukumbukirabe,
Mkazi wanga, moyo wanga,
Kusiyana kwathu inde sikunalili kwabwino,koma
Ndikungopempha kuti tibwererane .
(Outro)
Ndikufuna kukhalabe nawe,
Mu mtima mwanga, ndiwe wekha,
Tsopano, bwerera, bwerera,tabweleraaa iwe,tidzayambireso
Chikondi chathu.