Zakuwawani bwanji lelo dzana munayakhura zayine zambili
Ndelelo mwayamba kuyakhura zambili mwawona kuti azanu
Anditenga zakuwawani ndithu musanati ikomwele mbuzi
Kugunda galu galu akati abwezele muti yiphani galuyu
Wachita misala ayi sisita ndikawoneko Zina khariDwe rangali
Azanuso akaliwoneko pochoka munatukwana ose pamudzi
Ndinawoneka onyezaka thawiyija chifukwa chayinu amake
Junior pochoka samachoka choncho zimapangitsa kuti
Okhululuka asadzakhululukileni ndikaganiza zose zija
Munayakhura zija ine kukhosi bii akakuyese enawo tizawone
Mwina akakuzoloweni amake junior kwayine ayi ndinakutulukani
Sindifuna banja lomakharila kukanga ndikati ndiyende zavuta
Mafuso mbwee unapitakutiko unapita kuchibwezi iwee
Kodi phataosaka ndizawupeza kuine powopa kuphwanya
Lamulo junior koma chonde chonde inu musandiganizile
Zambiri ine ndimakasaka kuti panyumbapano tisamasowe
Rantchele ndikatelo akuti ndalakwitsa ndizawupeza kuti
Phata ine pakuti mukundikhomelela ndikapanda kugula ndiwo
Panyumba mwayambapo manong'o nong'o mwati sindidziwa
Kusaka chosecho kuyenda mukundiletsa inu kapena mwina ndimayeselo
A chikhara chodziwa kuti moyo wako ndiwotele make junior
Ndikanakusiya tilipachibwezi paja koma mphuno salota
Lelo tayimbila fiti manja
Uku ndikuyimba Kwa fanizo Kwa dowela