1. Msaiwale tsiku la Mbuye wathuyo.
Ndi tsiku lopambana masiku enawo;
Ndi tsiku lakupuma ndi la cimwemweco,
Kuwala kwace kuli kocoka mmwambamo.
CHORUS;
Tikondwera kudza kwa Sabata lacelo.
Tikondwera kudza kwa Sabata lacelo.
2. Sunga tsiku lace lopatulikalo,
Pembedza mwini njira yakunka mmwambamo;
Tikamtsatira Iye pa dziko linotu,
Adzatipatsa madzi a moyo wacewo.
3. Timyimbira Yesu pa tsiku lonseli,
Ambuye ali Bwenzi la ana onsewo.
Wokoma Mtima ndinu, Mukhale nafetu,
Munalonjeza kuti mudzadza mtimamu.