NDAIMA NJI
Chiyembekezo changacho
Chamagidwa pa Mwaziwo;
Sindikhulupira ena
Ndingotsamira pa yesu
Chorus
Ndaima nji pa Khristuyo
Ndiye chitanthwe cholimba
Maziko ena ndi mchenga.
Nkhope yake ‘kabisika
Ndipuma mchisomo chake;
M’namondwe ndi mphepo zonse
Nangula wanga ali nji.
Pangano lake m’Mwaziwo
Lindisunga m’chigumula,
Zondizinga zikachoka
Yesu ndiye tankthwe langa.
Likalira lipengalo
Ndipezeke mwa Yesuyo
Wovekedwa wolungama
Wopanda banga konseko.