1 Pemphero ndiko kufuna,
Kulakalakatu;
Ndi monga moto liyaka
Mumtima wa munthu.
2 Pemphero ndiko kulira,
Ngakhale misozi,
Kupenyetsetsa Kumwamba,
Mulungu mpafupi.
3 Pemphero ndiko kufuna
Kwa mwana wamng'ono;
Ndiponso mawu amphamvu
A munthu wamvanu.
4 Pemphero ndiwo mweyawo
Apuma akhristu;
Ndi mapemphero tilowa
Dziko la imfalo.
5 Mutiphunzitse, Mbuyathu,
Kupempha kotero,
Kuyandikira kwa Mlungu
Ndi mtima wabwino.